Exodus 38:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mthandizi wake Oholiyabu, mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, anali wodziŵa kuzokota miyala, kulemba mapulani, ndi kuwomba nsalu yopetedwa ndi thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira, ndiponso nsalu ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi pamodzi naye Oholiyabu, mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, ndiye wozokota miyala, ndi mmisiri waluso, ndiponso wopikula ndi lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pamodzi ndi Oholiabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, wa luso la zopangapanga ndi kulemba mapulani, ndi wopanga nsalu zolukidwa bwino za mtundu wa mtambo, yapepo ndi zofiira, zofewa ndi zosalala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi pamodzi naye Aholiabu, mwana wa Ahisama, wa pfuko la Dani, ndiye wozokota miyala, ndi mmisiri waluso, ndiponso wopikula ndi lamadzi ndi lofiira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.