Exodus 38:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Golide yense amene ankagwiritsa ntchito popanga malo opatulika, anali golide amene anthu adaapereka kwa Chauta, ndipo ankalemera makilogaramu 1,000, potsata miyeso ya ku Nyumba ya Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Golide yense anachita naye mu ntchito yonse ya malo opatulika, golide wa choperekacho, ndicho matalente makumi awiri kudza asanu ndi anai, ndi masekeli mazana asanu ndi awiri, kudza makumi atatu, monga mwa sekeli wa malo opatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Golide yense wochokera ku nsembe yoweyula amene anagwiritsa ntchito pa ntchito yonse yopanga malo wopatulika anali wolemera makilogalamu 1,000 potsata miyeso ya kumalo wopatulika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Golidi yense anacita naye mu nchito yonse ya malo opatulika, golidi wa coperekaco, ndico matalente makumi awiri kudza asanu ndi anai, ndi masekeli mazana asanu ndi awiri, kudza makumi atatu, monga mwa sekeli wa malo opatulika.