Exodus 38:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu aliyense ankapereka beka imodzi (ndiye kuti magaramu ngati 6, potsata muyeso wa ku Nyumba ya Mulungu.) Anthu onse olembedwa m'kaundula analipo 603,550 amuna okha, a zaka makumi aŵiri kapena kupitirira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu mmodzi anapereka beka, ndiwo limodzi la magawo awiri la sekeli, kuyesa sekeli wa malo opatulika, anatero onse akupita kunka kwa owerengedwawo, kuyambira munthu wa zaka makumi awiri ndi oposa, ndiwo anthu zikwi mazana asanu ndi limodzi kudza zitatu, ndi mazana asanu mphambu makumi asanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu aliyense amapereka beka imodzi, kufanana ngati makilogalamu 6, potsata muyeso wa ku malo wopatulika. Kuchokera kwa aliyense amene anawerengedwa kuyambira zaka 20 kapena kuposerapo, amuna onse analipo 603,550.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
munthu mmodzi anapereka beka, ndiwo limodzi la magawo awiri la sekeli, kuyesa sekeli wa malo opatulika, anatero onse akupita kumka kwa owerengedwawo, kuyambira munthu wa zaka makumi awiri ndi oposa, ndiwo anthu zikwi mazana asanu ndi limodzi kudza zitatu, ndi mazana asanu mphambu makumi asanu.