Exodus 38:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Siliva wolemera makilogaramu 3,400 adamangira masinde 100 a malo opatulika ndi a nsalu zochingira. Tsinde lililonse linkalira siliva wolemera makilogaramu 34.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo matalente zana limodzi a siliva ndiwo a kuyengera makamwa a malo opatulika, ndi makamwa a nsalu yotchinga; makamwa zana limodzi matalente zana limodzi, talente limodzi kamwa limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anagwiritsa ntchito siliva wolemera makilogalamu 3,400 kupanga matsinde 100 a ku malo wopatulika ndi makatani, ndipo makilogalamu 34 kupanga tsinde limodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo matalente zana limodzi a siliva ndiwo a kuyengera makamwa a malo opatulika, ndi makamwa a nsaru yocinga; makamwa zana limodzi matalente zana limodzi, talente limodzi kamwa limodzi.