Exodus 38:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndi makilogaramu otsalawo adapanga ngoŵe za pa nsanamirazo ndipo adakuta nsonga za nsanamira ndi kupanga mitanda yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapanga zokowera za mizati nsanamira ndi nsichi ndi masekeli aja chikwi chimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu asanu, nakuta mitu yake, nazigwirizitsana pamodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Makilogalamu otsalawo anagwiritsa ntchito popanga ngowe zamzati kukutira pamwamba pa mizati ndiponso kupanga zingwe zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapanga zokowera za mizati nsanamira ndi nsici ndi masekeli aja cikwi cimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu asanu, nakuta mitu yace, nazigwirizitsana pamodzi.