Exodus 38:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapanganso zipangizo zonse za guwalo, mbale zolandirira phulusa, mafosholo, mabeseni, ngoŵe zokoŵera zinthu, ndiponso ziwaya zosonkhapo moto. Zonsezo zidapangidwa ndi mkuŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anapanganso zipangizo zonse za guwalo, zotayira, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, ndi mitungo, ndi zopalira moto; zipangizo zake zonse anazipanga zamkuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anapanganso ziwiya zamkuwa izi zogwirira ntchito pa guwalo: miphika, mafosholo, mabeseni owazira magazi, ngowe zokowera nyama ndi zosonkhezera moto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anapanganso zipangizo zonse za guwalo, zotayira, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, ndi mitungo, ndi zoparira moto; zipangizo zace zonse anazipanga zamkuwa.