Exodus 38:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adapanga chitsulo cha sefa, cha guwa lansembelo, cholukidwa ndi mkuŵa wokhawokha, ndipo adachiika kunsi kwake kwa chibumi cha guwa, kuti chifike pakatimpakati pa guwalo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapangira guwa la nsembelo sefa, malukidwe ake nja mkuwa, pansi pa khoma lamkati lake wakulekeza pakati pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anapanga sefa yachitsulo chamkuwa ya guwa lansembelo kuti ikhale mmunsi mwa khoma la guwa lansembelo, kuchokera pansi mpaka pakati pa khoma la guwalo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapangira guwa La nsembelo made, malukidwe ace nja mkuwa, pansi pa matso ace wakulekeza pakati pace.