Exodus 38:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adapanga beseni lamkuŵa losambira, pamodzi ndi phaka lake. Adapanga zimenezi ndi akalilole a akazi amene ankatumikira ku chipata choloŵera m'chihema chamsonkhano chija, kumene Chauta ankakumanako ndi anthu ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la chihema chokomanako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anapanga beseni lamkuwa lokhala ndi miyendo yamkuwanso kuchokera ku magalasi oyangʼanira nkhope a amayi amene ankatumikira pa chipata cha tenti ya msonkhano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lace lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la cihema cokomanako.