Exodus 39:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adapanga zovala zokongola kwambiri za ansembe, zovala potumikira m'malo oyera. Adapanga zovalazo ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira. Adapanga zovala za Aroni monga momwe Chauta adalamulira Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaomba zovala zakutumikira nazo ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, atumikire nazo m'malo opatulika, naomba zovala zopatulika za Aroni; monga Yehova adamuuza Mose.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anapanga zovala za ansembe, zovala potumikira ku malo wopatulika pogwiritsa ntchito nsalu ya mtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira. Anapanganso zovala zopatulika za Aaroni monga momwe Yehova analamulira Mose.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaomba zobvala zakutumikira nazo ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, atumikire nazo m'malo opatulika, naomba zobvala zopatulika za Aroni; monga Yehova adamuuza Mose.