Exodus 39:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panali miyala khumi ndi iŵiri imene adalembapo maina a mafuko a Israele. Inali miyala khumi ndi iŵiri yozokotedwa ngati zidindo, ndipo mwala uliwonse unali ndi dzina la fuko limodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo miyalayi inakhala monga mwa maina a ana a Israele, khumi ndi awiri, monga mwa maina ao; ngati malochedwe a chosindikizira, yonse monga mwa maina ake, kwa mafuko khumi ndi awiriwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Miyalayo inalipo khumi ndi iwiri, uliwonse kuyimira dzina limodzi la ana a Israeli. Mwala uliwonse unazokotedwa ngati chidindo dzina limodzi la mafuko khumi ndi awiri a Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo miyalayi inakhala monga mwa maina a ana a Israyeli, khumi ndi awiri, monga mwa maina ao; ngati malocedwe a cosindikizira, yonse monga mwa maina ace, kwa mafuko khumi ndi awiriwo.