Exodus 39:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapanganso mphete ziŵiri zagolide, nazilumikiza ku mbali yam'munsi, kutsogolo kwa tizikwewo tam'mapewa ta chovala cha efodi chija, pafupi ndi msoko, ndiponso pamwamba pa lamba woluka mwaluso uja wa efodiyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolide, naziika pa zapamapewa ziwiri za efodi pansi pake, pa mbali yake ya kutsogolo, pafupi pa msoko wake, pamwamba pa mpango wa efodi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anapanga mphete zina ziwiri zagolide ndi kuzilumikiza kumunsi kwa tinsalu takutsogolo kwa efodi, pafupi ndi msoko, pamwamba pangʼono pa lamba wamʼchiwuno wa efodi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolidi, naziika pa zapamapewa ziwiri za efodi pansi pace, pa mbali yace ya kutsogolo, pafupi pa msoko wace, pamwamba pa mpango wa efodi.