Exodus 39:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adalumikiza mphete za chovala chapachifuwa zija ku mphete za efodi. Adalumikiza ndi kamkuzi kobiriŵira, kuti chovala chapachifuwacho chikhale pamwamba pa lamba woluka mwaluso uja, ndipo chisalekane ndi efodi ija, monga momwe Chauta adalamulira Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamanga chapachifuwa pa mphete zake ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti chikhale pa mpango wa efodi, ndi kuti chapachifuwa chisamasuke paefodi; monga Yehova anamuuza Mose.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anamangirira mphete za pa chovala chapachifuwa zija ku mphete za efodi ndi chingwe chamtundu wa mtambo, kulumikiza lamba ndi chovala chapachifuwacho kuti chovala chapachifuwacho chisalekane ndi efodi ija monga Yehova analamulira Mose.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamanga capacifuwa pa mphete zace ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti cikhale pa mpango wa efodi, ndi kuti capacifuwa cisamasuke paefodi; monga Yehova anamuuza Mose.