Exodus 39:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono panali khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, kuzungulira mpendero wonse wa mkanjo, umene ansembe ankavala pogwira ntchito zaunsembe, monga momwe Chauta adalamulira Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mliu ndi khangaza, mliu ndi khangaza pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, kutumikira nazo; monga Yehova anamuuza Mose.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero panali mphonje imodzi ndi belu limodzi kuzungulira mpendero wa mkanjo wovala potumikira monga momwe Yehova analamulira Mose.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mliu ndi khangaza, mliu ndi khangaza pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, kutumikira nazo; monga Yehova anamuuza Mose.