Exodus 39:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adasula golide mwaphanthiphanthi, namlenzalenza, kuti amlukire kumodzi ndi thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira, ndiponso la bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ntchito yaumisiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anasula golide waphanthiphanthi, nalemba nsambo, kuti amuombe pamodzi ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya mmisiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anasula golide wopyapyala ndi kumulezaleza kuti alumikize kumodzi ndi nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yosalala yofewa yolukidwa mwaluso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anasula golidi waphanthiphanthi, nalemba nsambo, kuti amuombe pamodzi ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya mmisiri.