Exodus 39:41 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adabweranso ndi zovala zokongola kwambiri zoyenera kuvala ansembe potumikira m'malo oyera, zovala zopatulika za wansembe Aroni, ndiponso zovala za ana ake aamuna, zoyenera kuzivala pogwira ntchito zaunsembe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
zovala zokoma za kutumikira nazo m'malo opatulika, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, kuchita nazo ntchito ya nsembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndiponso zovala zolukidwa zovala potumikira kumalo opatulika, zovala zopatulika za wansembe, Aaroni pamodzi ndi za ana ake aamuna pamene akutumikira monga ansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
zobvala zokoma za kutumikira nazo m'malo opatulika, ndi zobvala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zobvala za ana ace, kucita nazo nchito ya usembe.