Exodus 39:43 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mose adaona zonse zimene zidapangidwazo, ndipo adatsimikiza kuti adazipangadi monga momwe Chauta adalamulira. Pamenepo Mose adaŵadalitsa anthu onsewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anaona ntchito zonse, ndipo, taonani, adaichita monga Yehova adamuuza, momwemo adachita. Ndipo Mose anawadalitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anayendera ntchitoyo ndipo anaona kuti anayichita monga momwe Yehova analamulira. Kotero Mose anawadalitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anaona nchito zonse, ndipo, taonani, adaicita monga Yehova adamuuza, momwemo adacita. Ndipo Mose anawadalitsa.