Exodus 39:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panalinso lamba woluka mwaluso, womangira efodi, wolukira kumodzi ndi efodiyo. Lambayo nayenso anali wa nsalu yagolide, ndi wa nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso wa bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, monga momwe Chauta adalamulira Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mpango wa efodi wokhala pamenepo, wakummanga nao unali woombera kumodzi wa chiombedwe chomwechi; wa golide, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; monga Yehova adauza Mose.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lamba womangira efodi anali wolukidwa mwaluso ngati efodiyo. Anali nsalu imodzi ndi efodiyo, wopangidwa ndi golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala, monga momwe Yehova analamulira Mose.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mpango wa efodi wokhala pamenepo, wakummanga nao unali woombera kumodzi wa ciombedwe comweci; wa golidi, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; monga Yehova adauza Mose.