Exodus 39:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka adakonza miyala yakongola ya mtundu wa onikisi, naikhazika m'zoikamo zake zagolide. Tsono adaizokota monga amachitira pa chidindo, nalembapo mozokota bwino maina onse a ana aamuna a Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anakonza miyala yasohamu, yogwirika m'zoikamo zagolide, yolocha ngati malochedwe a chosindikizira, ndi maina a ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anakonza miyala ya onikisi ndi kuyiika mu zoyikamo zake zagolide ndipo anazokota mayina a ana a Israeli monga amachitira pa chidindo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anakonza miyala yasohamu, yogwirika m'zoikamo zagolidi, yoloca ngati malocedwe a cosindikizira, ndi maina a ana a lsrayeli.