Exodus 4:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adati, “Pepani Chauta, ndapota nanu, ine sindidziŵa kulankhula bwino chiyambire kale, kapena kuyambira paja mwayamba kulankhula nane mtumiki wanune. Lilime langa ndi lolemera, ndine wachibwibwi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anati kwa Yehova, Mverani, Ambuye, ine ndine munthu wosowa ponena, kapena dzulo, kapena kale, kapena chilankhulire Inu ndi kapolo wanu, pakuti ndine wa m'kamwa molemera, ndi wa lilime lolemera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anati kwa Yehova, “Chonde Ambuye, chikhalire ine ndakhala munthu wosatha kuyankhula bwino. Ngakhale tsopano pamene mukundiyankhula, lilime langa ndi lolemera. Ndine wachibwibwi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anati kwa Yehova, Mverani, Ambuye, ine ndine munthu wosowa ponena, kapena dzulo, kapena kale, kapena cilankhulire Inu ndi kapolo wanu, pakuti ndine wa m'kamwa molemera, ndi wa lilime lolemera.