Exodus 4:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Chauta adafunsa Mose kuti, “Kodi adapatsa munthu pakamwa ndani? Ndani amasandutsa munthu kuti akhale wosamva kapena wosalankhula, wopenya kapena wosapenya? Kodi si ndine Chauta amene ndimachita zimenezo?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yehova ananena naye, Anampangira munthu m'kamwa ndani? Kapena analenga munthu wosalankhula ndani, kapena wogontha, kapena wamaso, kapena wakhungu? Si ndine Yehova kodi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anati kwa iye, “Kodi anapatsa munthu pakamwa ndani? Ndani amasandutsa munthu kuti akhale wosayankhula kapena wosamva? Ndani amapanga munthu kukhala wopenya kapena wosaona? Kodi si Ine Yehova?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yehova ananena naye, Anampangira munthu m'kamwa ndani? Kapena analenga munthu wosalankhula ndani, kapena wogontha, kapena wamaso, kapena wakhungu? Si ndine Yehova kodi?