Exodus 4:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pompo Chauta adamkalipira Mose, namufunsa kuti, “Bwanji mbale wako Aroni, Mlevi uja? Ndikudziŵa kuti angathe kulankhula bwino kwambiri. Iyeyo akubwera kudzakumana nawe, ndipo adzakondwa kwambiri pokuwona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mkwiyo wa Yehova unamyakira Mose, ndipo anati, Nanga Aroni Mlevi mbale wako sialipo kodi? Ndidziwa kuti kulankhula alankhula. Ndipo, taona, atuluka kudzakomana ndiwe; ndipo pakuona iwe adzakondwera m'mtima mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yehova anamupsera mtima Mose ndipo anati, “Kodi suli ndi mʼbale wako Aaroni wa fuko la Levi? Ine ndikudziwa kuti iye amayankhula bwino. Iye wanyamuka kale kudzakumana nawe ndipo adzasangalala akadzakuona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mkwiyo wa Yehova unamyakira Mose, ndipo anati, Nanga Aroni Mlevi mbale wako sialipo kodi? Ndidziwa kuti kulankhula alankhula. Ndipo, taona, aturuka kudzakomana ndiwe; ndipo pakuona iwe adzakondweram'mtima mwace.