Exodus 4:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mose adabwerera kwa Yetero mpongozi wake uja, namuuza kuti, “Chonde mundilole kuti ndibwerere ku Ejipito kwa abale anga, kuti ndikaŵaone ngati ali moyo.” Yetero adauza Mose kuti, “Pitani ndi mtendere.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anabwera namuka kwa Yetero mpongozi wake, nanena naye, Ndimuketu, ndibwerere kunka kwa abale anga amene ali m'Ejipito, ndikaone ngati akali ndi moyo. Ndipo Yetero ananena ndi Mose, Pita bwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Mose anabwerera kwa Yetero, mpongozi wake ndipo anati kwa Iye, “Chonde ndiloleni kuti ndibwerere ku Igupto kwa anthu anga kuti ndikaone ngati ali moyo.” Yeteri anati, “Pitani mu mtendere.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anabwera namuka kwa Yetero mpongozi wace, nanena naye, Ndimuketu, ndibwerere kumka kwa abale anga amene ali m'Aigupto, ndikaone ngati akali ndi moyo. Ndipo Yetero ananena ndi Mose, Pita bwino.