Exodus 4:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Mose adatenga mkazi wake ndi ana ake, naŵakweza pa bulu onsewo, ndipo adapita ku Ejipito, atatenga ndodo imene adampatsa Mulungu ija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake amuna, nawakweza pa bulu, nabwerera kunka ku dziko la Ejipito; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, ndipo anawakweza pa bulu nayamba ulendo wobwerera ku Igupto. Ndipo anatenga ndodo ya Mulungu ija mʼdzanja lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Mose anatenga mkazi wace ndi ana ace amuna, nawakweza pa buru, nabwerera kumka ku dziko la Aigupto; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lace.