Exodus 4:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adauzanso Mose kuti, “Pamene ukubwerera ku Ejipito, ukachite ndithu pamaso pa Farao zozizwitsa zonse zimene ndakuuza kuti ukachite. Koma ndidzamuumitsa mtima, ndipo sadzalola kuti anthu anga apite.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kunka ku Ejipito, usamalire uchite zozizwa zonse ndaziika m'dzanja lako, pamaso pa Farao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wake kuti asadzalole anthu kupita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anati kwa Mose, “Ukaonetsetse kuti wachita pamaso pa Farao zodabwitsa zonse zimene ndayika mphamvu mwa iwe kuti ukachite. Koma Ine ndidzawumitsa mtima wake kotero kuti sadzalola anthuwo kuti apite.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kumka ku Aigupto, usamalire ucite zozizwa zonse ndaziika m'dzanja lako, pamaso pa Farao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wace kuti asadzalole anthu kupita.