Exodus 4:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Zipora adatenga mwala wakuthwa, naumbala mwana wake, ndipo khungulo adalikhudzitsa m'miyendo mwa Mose. Kenaka Ziporayo adati, “Zoonadi, iwe ndiwe mkwati woomboledwa ndi magazi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Zipora anatenga mpeni wamwala, nadula khungu la mwana wake, naliponya pa mapazi ake; nati, Pakuti iwe ndiwe mkwati wanga wamwazi. Ndipo Iye anamleka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Zipora anatenga mwala wakuthwa nachita mdulidwe mwana wake ndipo khungulo analikhudzitsa pa mapazi a Mose. Iye anati “Zoonadi, kwa ine ndiwe mkwati wamagazi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Zipora anatenga mpeni wamwala, nadula khungu la mwana wace, naliponya pa mapazi ace; nati, Pakuti iwe ndiwe mkwati wanga wamwazi. Ndipo iye anamleka.