Exodus 4:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Chauta adamleka Mose osamupha. Ndiye pamene Zipora adanena kuti, “Ndiwe mkwati woomboledwa ndi magazi,” chifukwa cha kuumbalako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anati mkaziyo, Mkwati wamwazi iwe, chifukwa cha mdulidwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yehova anamuleka Mose wosamupha. Pa nthawiyo, Zipora anati, “Mkwati wa magazi,” ponena za mdulidwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anati mkaziyo, Mkwati wamwazi iwe, cifukwa ca mdulidwe.