Exodus 4:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Aisraele aja adakhulupiriradi zimenezo. Tsono atamva kuti Chauta adadzaŵayendera ndipo kuti adaona kuzunzika kwaoko, adaŵeramitsa mitu pansi napembedza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthuwo anakhulupirira; ndipo pamene anamva kuti Yehova adawazonda ana a Israele, ndi kuti adaona mazunzo ao, anawerama, nalambira Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo anakhulupirira. Iwo atamva kuti Yehova anadzawayendera ndi kuti waona mmene akuzunzikira, anaweramitsa mitu pansi napembedza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthuwo anakhulupirira; ndipo pamene anamva kuti Yehova adawazonda ana a Israyeli, ndi kuti adaona mazunzo ao, anawerama, nalambira Mulungu.