Exodus 4:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adamuuza kuti, “Ukachite zimenezi, ndipo adzakhulupirira kuti Chauta, Mulungu wa makolo ao, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, Mulungu wa Yakobe, adakuwonekeradi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti akhulupirire kuti wakuonekera Yehova Mulungu wa makolo ao, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anati, “Ukachite zimenezi ndipo akakukhulupirira kuti Yehova, Mulungu wa makolo awo, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo, wakuonekera iwe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti akhulupirire kuti wakuonekera Yehova Mulungu wa makolo ao, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo.