Exodus 4:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adauzanso Mose kuti, “Tapisa dzanja lako m'malayamo.” Iye adapisadi. Koma potulutsa dzanjalo, linali lakhate, lotuŵa ngati ufa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova ananenanso naye, Longa dzanja lako pachifuwa pako. Ndipo analonga dzanja lake pachifuwa pake, nalitulutsa, taonani, dzanja lake linali lakhate, lotuwa ngati chipale chofewa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anatinso, “Pisa dzanja lako mʼmalaya akowo.” Choncho Mose anapisa dzanja lake mʼmalaya ake ndipo pamene analitulutsa, linali la khate kuchita kuti mbuu ngati ufa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova ananenanso naye, Longa dzanja lako pacifuwa pako. Ndipo analonga dzanja lace pacifuwa pace, naliturutsa, taonani, dzanja lace linali lakhate, lotuwa ngati cipale cofewa.