Exodus 4:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adati, “Lipisenso m'malayamo dzanja lakolo.” Iye adalipisanso ndipo potulutsa, linali labwinobwino lopanda khate, koma lofanana ndi thupi lake lonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena iye, Bwerezanso dzanja lako pachifuwa pako. Ndipo anabwerezanso dzanja lake pachifuwa pake; nalitulutsa pachifuwa pake, taonani, linasandukanso lomwe lakale.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anati, “Tsopano pisanso dzanja lako mʼmalaya.” Mose anapisanso dzanja lakelo mʼmalaya ake ndipo atalitulutsa, linali labwinobwino, ngati thupi lake lonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena iye, Bwerezanso dzanja lako pacifuwa pako. Ndipo anabwerezanso dzanja lace pacifuwa pace; naliturutsa pacifuwa pace, taonani, linasandukanso lomwe lakale.