Exodus 4:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma akakapanda kukhulupirira zizindikiro ziŵiri zonsezo, osafuna kumva zomwe ukaŵauzezo, ukatenge madzi a mu mtsinje wa Nailo, ukaŵathire pa nthaka youma. Madzi amenewo akasanduka magazi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzatero, akapanda kukhulupirira zingakhale zizindikiro izi, ndi kusamvera mau ako, ukatunge madzi a kunyanja ndi kuthira pamtunda; ndi madzi watunga ku nyanjayo adzasanduka mwazi pamtunda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati sakakhulupirira zizindikiro ziwiri izi kapena kukumvera, ukatunge madzi a mu mtsinje wa Nailo ndi kuwathira pa mtunda powuma ndipo madziwo adzasanduka magazi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzatero, aka panda kukhulupirira zingakhale zizindikilo izi, ndi kusamvera mau ako, ukatunge madzi a kunyanja, ndi kuthira pamtunda; ndi madzi watunga ku nyanjayo adzasanduka mwazi pamtunda.