Exodus 40:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono udzozenso guwa loperekapo nsembe zopsereza, pamodzi ndi zipangizo zake zomwe. Guwalo ulipereke kwa Mulungu, kuti likhale loyera ndipo lidzakhaladi loyera kopambana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo udzoze guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zake zonse, ndi kulipatula guwalo; ndipo guwalo lidzakhala lopatulika kwambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka udzoze guwa lansembe lopsereza ndi ziwiya zake zonse. Ulipatule guwalo ndipo lidzakhala loyera kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo udzoze guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zace zonse, ndi kulipatula guwalo; ndipo guwalo lidzakhala lopatulikitsa.