Exodus 40:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aroniyo umuveke zovala zopatulika. Umdzoze, ndipo umpatule kuti akhale wansembe wonditumikira Ine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nuveke Aroni chovala zopatulikazo; ndi kumdzoza, ndi kumpatula andichitire Ine ntchito ya nsembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka umuveke Aaroni zovala zopatulika, umudzoze ndi kumupatula kotero kuti athe kunditumikira monga wansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nubveke Aroni cobvala zopatulikazo; ndi kumdzoza, ndi kumpatwa andicitire Ine nchito ya nsembe.