Exodus 40:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono uŵadzoze monga momwe udadzozera bambo wao, kuti akhale ansembe onditumikira Ine. Kudzozedwako kudzaŵasandutsa ansembe pa mibabwo ndi mibadwo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nuwadzoze, monga unadzoza atate wao, kuti andichitire ntchito ya nsembe; ndi kudzozedwa kwao kuwakhalire unsembe wosatha mwa mibadwo yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uwadzoze monga momwe unadzozera abambo awo, kotero kuti anditumikire monga ansembe. Kudzozedwako kudzakhala unsembe wawo pa mibado ndi mibado”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nuwadzoze, monga unadzoza atate wao, kuti andicitire nchito ya nsembe; ndi kudzozedwa kwao kuwakhalire unsembe wosatha mwa mibadwo yao.