Exodus 5:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Mose ndi Aroni adapita kwa Farao nakamuuza kuti, “Naŵa mau a Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Uŵalole anthu anga apite ku chipululu, kuti akachite mwambo wachipembedzo wondilemekeza Ine.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m'chipululu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zitachitika izi, Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndipo anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Aloleni anthu anga apite, kuti akachite chikondwerero cha Ine mʼchipululu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pambuyo pace Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, Lola anthu anga apite, kundicitira madyerero m'cipululu.