Exodus 5:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akulu a Farao aja ogwiritsa ntchito, adafulumizitsa Aisraele naŵauza kuti, “Muziwumba chiŵerengero chonchija cha njerwa pa tsiku, monga munkachitira pamene ankakupatsani udzu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akufulumiza anawakakamiza, ndi kuti, Tsirizani ntchito zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake, monga muja munali ndi udzu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akapitawo a thangata aja anawafulumiza anthu aja nati, “Malizani kugwira ntchito yanu ya tsiku ndi tsiku monga mmene zinalili pamene munkapatsidwa udzu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akufulumiza anawakakamiza, ndi kuti, Tsirizani nchito zanu, nchito ya tsiku pa tsiku lace, monga muja munali ndi udzu.