Exodus 5:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akuluakulu a thangata a Farao aja ankamenyanso akapitao Achiisraele amene adaŵaika kuti akhale omayang'anira ntchito, namaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani lero simudaumbe chiŵerengero chonchija cha njerwa monga munkachitira kale?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapanda akapitao a ana a Israele, amene ofulumiza a Farao adawaika, ndi kuti, Nanga dzulo ndi lero simunatsiriza bwanji ntchito yanu yoneneka ya njerwa, monga kale?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akapitawo a thangata a Farao ankawamenya oyangʼanira anzawo a Chiisraeli aja nawapanikiza kuti, “Chifukwa chiyani lero simunawumbe chiwerengero chovomerezeka cha njerwa monga chakale chija?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapanda akapitao a ana a Israyeli, amene ofulumiza a Farao adawaika, ndi kuti, Nanga dzulo ndi lero simunatsiriza bwanji nchito yanu yoneneka ya njerwa, monga kale?