Exodus 5:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akapitao achiisraele aja adaona kuti alidi pa mavuto, ataŵauza kuti, “Muziwumba chiŵerengero chonchija cha njerwa tsiku ndi tsiku.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akapitao a ana a Israele anaona kuti kudawaipira, pamene ananena, Musamachepetsa njerwa zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Oyangʼanira anzawo a Chiisraeli anazindikira kuti ali pa mavuto pamene anawuzidwa kuti, “Musachepetse chiwerengero cha njerwa chimene muyenera kuwumba tsiku lililonse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akapitao a ana a Israyeli anaona kuti kudawaipira, pamene ananena, Musamacepetsa njerwa zanu, nchito ya tsiku pa tsiku lace.