Exodus 5:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Farao adayankha kuti, “Kodi Chautayo ndani kuti ine nkumvera zimenezo ndi kuŵalola Aisraele kuti apite? Chautayo sindimdziŵa, ndipo sindidzalola konse kuti Aisraele apite.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Farao anati, Yehova ndani, kuti ndimvere mau ake ndi kulola Israele apite? Sindimdziwa Yehova, ndiponso sindidzalola Israele apite.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Farao anati, “Yehova ndani kuti ine ndimumvere ndi kulola Aisraeli kuti apite? Ine Yehova sindikumudziwa ndipo sindilola kuti Aisraeli apite.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Farao anati, Yehova ndani, kuti ndimvere mau ace ndi kulola Israyeli apite? Sindimdziwa Yehova, ndiponso sindidzalola Israyeli apite.