Exodus 5:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo adaŵauza kuti, “Chauta aone mwachitazi, ndipo akuweruzeni inu poti Farao ndi nduna zake mwaŵasandutsa adani athu. Inuyo ndinu amene mwaika lupanga m'manja mwao kuti atiphe ife.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ananena nao, Yehova akupenyeni, naweruze; pakuti mwatinyansitsa pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndi kuwapatsa lupanga m'dzanja lao kutipha nalo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo iwo anati, “Yehova akupenyeni ndi kukuweruzani popeza mwachititsa Farao ndi nduna zake kuti anyansidwe nafe ndipo mwayika lupanga mʼmanja mwawo kuti atiphe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ananena nao, Yehova akupenyeni, naweruze; pakuti mwatinyansitsa pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ace, ndi kuwapatsa lupanga m'dzanja lao kutipha nalo.