Exodus 5:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma chiŵerengero cha njerwa chikhale chonchija, monga momwe ankaumbira kale. Musaŵachepetsere ndi pang'ono pomwe, ngaulesi ameneŵa. Nchifukwa chake akulira nkumati, ‘Tiyeni tikapereke nsembe kwa Mulungu wathu.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo muziwawerengera njerwa, monga momwe anapanga kale; musachepsapo, popeza achita chilezi; chifukwa chake alikufuula, ndi kuti, Timuke, timphere nsembe Mulungu wathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma musawachepetsere chiwerengero cha njerwa chomwe munawalamulira kale kuti aziwumba. Iwowa ndi aulesi. Nʼchifukwa chake akulira kuti, ‘Tiloleni tipite tikapereke nsembe kwa Mulungu wathu.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo muziwawerengera njerwa, monga momwe anapanga kale; musacepsapo, popeza acita cilezi; cifukwa cace alikupfuula, ndi kuti, Timuke, timphere nsembe Mulungu wathu.