Exodus 6:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adauza Moseyo kuti, “Uwona tsopano zimene ndimchite Farao. Ndidzakakamiza Farao kuti atulutse anthu anga m'dziko lake. Ndithudi, adzaŵatulutsiratu m'dzikomo, chifukwa ndidzamkakamiza ndi dzanja langa lamphamvu. Zoonadi, dzanja langa lamphamvu lidzamuumiriza kuti aŵapirikitse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona chomwe ndidzachitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m'dziko lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anawuza Mose kuti, “Tsopano udzaona zimene ndimuchite Farao: Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzalola anthu anga kuti atuluke. Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzawatulutsa mʼdziko lake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona comwe ndidzacitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m'dziko lace.