Exodus 6:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Mose adauza Chauta kuti, “Ngati Aisraele enieniwo sandimvera ine, nanji Farao angandimvere bwanji? Inetu paja sindikhoza kulankhula bwino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Mose ananena pamaso pa Yehova, ndi kuti, Onani, ana a Israele sanandimvere ine; adzandimvera bwanji Farao, ndine wa milomo yosadula?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Mose ananena kwa Yehova kuti, “Ngati Aisraeli sanandimvere, Farao akandimvera chifukwa chiyani, pajatu sinditha kuyankhula bwino?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Mose ananena pamaso pa Mulungu, ndi kuti, Onani, ana a Israyeli sanandimvera ine; adzandimvera bwanji Farao, ndine wa milomo yosadula?