Exodus 6:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Naŵa atsogoleri a mabanja a makolo ao. Ana a Rubeni, mwana wachisamba wa Israele, anali aŵa: Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. Ameneŵa ndiwo a m'banja la Rubeni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akulu a mbumba za makolo ao ndi awa: ana amuna a Rubeni, woyamba wa Israele ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi; amene ndiwo mabanja a Rubeni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atsogoleri a mafuko awo anali awa: Ana a Rubeni mwana wachisamba wa Israeli anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. Awa anali mafuko a Rubeni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akuru a mbumba za makolo ao ndi awa: ana amuna a Rubeni, woyamba wa Israyeli ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezroni, ndi Karmi; amene ndiwo mabanja a Rubeni.