Exodus 6:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amuramu adakwatira mlongo wa bambo wake dzina lake Yokebede. Yokebedeyo adabala Aroni ndi Mose. Amuramu adakhala zaka 137 ali moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Amuramu anadzitengera Yokebede mlongo wa atate wake akhale mkazi wake; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amuramu ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amramu anakwatira Yokobedi mlongo wa abambo ake, amene anabereka Aaroni ndi Mose. Amramu anakhala ndi moyo kwa zaka 137.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Amramu anadzitengera Yokobedi mlongo wa atate wace akhale mkazi wace; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amramu ndizo zaria limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.