Exodus 6:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Eleazara mwana wa Aroni adakwatira mmodzi mwa ana a Putiyele, amene adamubalira Finehasi. Ameneŵa ndiwo atsogoleri a mabanja a Alevi malinga ndi mafuko ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana akazi a Putiyele akhale mkazi wake, ndipo anambalira Finehasi. Amenewo ndi akulu a makolo a Alevi mwa mabanja ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Eliezara mwana wa Aaroni anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Putieli, ndipo anabereka Finehasi. Awa anali atsogoleri a mabanja a Levi, monga mwa mafuko awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana akazi a Putieli akhale mkazi wace, ndipo anambalira Pinehasi. Amenewo ndi akuru a makolo a Alevi mwa mabanja ao.