Exodus 7:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ukamuuze Farao kuti Chauta, Mulungu wa Ahebri, wandituma kwa inu kuti ndikuuzeni mau aŵa: ‘Uŵalole anthu anga apite, akandipembedze ku chipululu. Koma mpaka tsopano lino sudandimverebe.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri anandituma kwa inu, ndi kuti, Lola anthu anga amuke kuti anditumikire m'chipululu; koma, taona, sunamvera ndi pano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ukamuwuze Farao kuti, ‘Yehova, Mulungu wa Ahebri wandituma kuti ndikuwuzeni kuti: Lolani anthu anga apite kuti akandipembedze mʼchipululu. Koma mpaka tsopano inu simunandimvere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri anandituma kwa inu, ndi kuti, Lola anthu anga amuke kuti anditumukire m'cipululu; koma, taona, sunamvera ndi pano.