Exodus 7:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene Chauta akunena ndi izi, akuti ‘Poona zimene ndichite, udzadziŵa kuti Ine ndinedi Chauta. Taona, ndidzamenya madzi a mu mtsinjewu ndi ndodo ili m'manja mwangayi, ndipo madzi onseŵa adzasanduka magazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova, Ndi ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova; taonani, ndidzapanda madzi ali m'nyanja ndi ndodo ili m'dzanja langa, ndipo adzasanduka mwazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Izi ndi zimene Yehova akunena: Ndi ndodo imene ili mʼdzanja langa ndidzamenya madzi a mu Nailo, ndipo madzi adzasanduka magazi. Ndikadzachita ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova, Ndi ici udzadziwa kuti Ine ndine Yehova: taonani, ndidzapanda madzi ali m'nyanja ndi ndodo iri m'dzanja langa, ndipo adzasanduka mwazi.