Exodus 7:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zonse zimene ndakulamulazi ukazinene, ndipo iye ndiye akauze Farao kuti aŵalole Aisraele kutuluka m'dziko mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwe uzilankhula zonse ndikulamulira; ndi Aroni mkulu wako azilankhula kwa Farao, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe ukanene zonse zimene ndakulamulirazi, ndipo Aaroni mʼbale wako ndiye akaziyankhule kwa Farao kuti atulutse ana a Israeli mʼdziko la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwe uzdankhula zonse ndikulamulira; ndi Aroni mkuru wako azilankhula kwa Farao, kuti alole ana a Israyeli aturuke m'dziko lace.