Exodus 7:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nsomba zonse zamumtsinjemo zidafa, ndipo kununkha kwake kwa madziwo kunali kwakuti Aejipito sadathenso kuŵamwa. Ndipo munali magazi okhaokha m'dziko lonse la Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi nsomba za m'nyanjamo zinafa; ndi nyanjayo inanunkha; ndipo Aejipito sanakhoze kumwa madzi a m'nyanjamo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nsomba za mu Nailo zinafa ndipo mtsinje unanunkha kwambiri kotero kuti Aigupto sanathe kumwa madzi ake. Magazi anali ponseponse mu Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi nsomba za m'nyanjamo zinafa; ndi nyanjayo inanunkha; ndipo Aaigupto sanakhoza kumwa madzi a m'nyanjamo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Aigupto.